Uthenga wa chipulumutso

Uthenga wa chipulumutso Landirani uthenga wabwino omasula. Ophutsitsa ndi odziwitsa. Ife ndife abale Anu mwa Ambuye.

20/04/2026

Azimayi ambiri akuvulidwa Ndi ma prophet NDI azibusa mu dzina lá mapemphero. Azimayi ndati ndikucheniezeni. Kulibe odzozedwa WA Mulungu angakuuze Kuti Mulungu akundilankhura Kuti ndigone nanu. Ameneyi NDI odzozedwa WA satana. Yesani mizimu ngati ichokera Kwa Mulungu

20/04/2026

Pepani aprophet athu. Kuti mukhale prophet munachita kakhwima. Munapeleka nsembe mwana osadziwa mwamuna. Munandira mphavu za kulozera Ndi kuchiza. Lelo ndinu man of God. Chonsecho mukuzidziwa inuyo Kuti sinu Munthu WA Mulungu. Lelo NDI umu mukungogona ndi azikazi ayeni Ake.

Pamene mukuchita chigololo mpamene mphavu zanu zikuchulukila. Dzivele chisoni prophet iwe. Azimiyoso Chenjerani NDI fisi uyo wangodzora ufa. Muthaweni akusakazani.

14/04/2026

Iwo amene adzipatulitsa nadziyeretsa, kuti amuke kuminda tsatanetsatane, ndi kudya nyama ya nkhumba, ndi chonyansa, ndi mbewa, adzathedwa pamodzi, ati Yehova.
(Yesaya 66:17)

Winatu Adana nawo uthengau

12/04/2026

Komatu Izi zomamuuza Munthu amene akufuna kulapa Kuti ayanjane NDI Ambuye. Ndi kumukana kumulandira ndikumuuza Kuti ukalape pawekha uko. Kapena tikamayimba nyimbo za worship iweyo udzilapa wekha uko. Kodi mukuzidziwa Kuti abusa mukulephera tchito yanu??? Ndipo ngati Akhristu anu onse adutsa pa njira imeneyi nkumati anamulandira Yesu. Anthuwo mwawasokeletsa. Simunawafikitse Kwa Ambuye. Avekele takulandirani khalani omasuka. Amasuka bwanji Munthu asanalape??

05/04/2026

LERO KHRISTU ADAUKA
Lero Khristu anauka,
Ndilo tsiku lokondwera
Iye kale anafera naombola otayika,
Haluluya, haleluya, haleluya, haleluya.

Tiyimbire zomtamira
Ndiye Khristu wa Kumwamba,
Natsikirako kumanda, nalanditsa auipa,
Haluluya, haleluya, haleluya, haleluya

Koma masautso ake anatiombola ife,
Ndiye Mfumu ya mafumu,
Mwana ndithu wa Mulungu.
Haluluya, haleluya, haleluya, haleluya.

Tiyimbire Mlungu wathu, kuti atikonda ndithu,
Mtamenso angelo inu,
Ndiye Tate, Mwana, Mzimu.
Haluluya, haleluya, haleluya, haleluya.



Shared from Chitsitsimutso Mobile App

05/04/2026

Nkhondo yatha imfa yagonja. Yesu wagonjetsa imfa. Palibeso manhã NDI imfa. Oro tife tidzakhalaso NDI moyo. Chikondwelelero ku dziko lapansi. Yesu wauka. Wina uyo zikumuwawa.

05/04/2026

Mateyu 28:18Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pa dziko lapansi. 19Cifukwa cace mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: 20ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu; ndipo onani, Ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira cimariziro ca nthawi ya pansi pano.

05/04/2026

NKHONDOYO YATHA

Nkhondoyo yatha, imfa yagonja,
Yesu wamoyo anaiposa,
Msampha woipa wonse naonja,
Aleluya!

Mphamvu za imfa ndi ZA Satana
Naye Ambuye zinalimbana,
Komatu Yesu anapambana
Aleluya!

Atha masiku aja ansoni,
Mbuye wauka, ali ndi mboni,
Lero chimwemwe, chatha chisoni,
Aleluya!

Nsinga za imfa Iye nadula,
Khomo la m’Mwamba nalitsegula,
Yesu timtama, tonse tifuula,
Aleluya!

Mbuye, mabala anu olimba,
Atichotsera mantha a imfa,
Tsono ndi mtima wonse tiyimba,
Aleluya!



Shared from Chitsitsimutso Mobile App

04/04/2026

Pasulani kachisiyu ine ndidzamanga wina masiku Atatu. kuyamba .👉 Friday.👉 Saturday 👉 Sunday kutsilizidwa. Yesu wauka. Ndilo tsiku lokondwera. Mwana wazioni konzekerani tivine mawa kachisi wathu watsilizidwa. Chikondwelelero padziko lonse lapansi patsikuli.

yohane 2:19 Yesu anayankha nati kwa iwo, Pasulani kacisi uyu, ndipo masiku atatu ndidzamuutsa. 2

04/04/2026

Dzulo (Friday) Yesu anapachikidwa pamtanda. Lelo (Saturday) anakhala Ali manda. Mawa (Sunday) anauka Kwa akufa mamawa nauza ophunzira Kuti pitani tikakumane ku galileya. Kunali chikondwelelero chachikulu patsikuli. Zonse zinayambira pamenepa. Kusonkhana Kwa tsiku loyamba la sabata. Pamene Anzathu ena anali ndwii. Zoti mawa kuli chisangalaro chachikulu Iwo sanadziwe. tchito kugula zigawenga Kuti zizinena Kuti Yesu sanauke adzamuba ophunzira Ake. Cholinga ayipitse mbili yake.

14/12/2025

Yobu 31.1
"Ndinachita pangano ndi maso anga sindidzaona namwali momusilira"

lero yambani kukhutitsidwa ndi banja lomwe Mulungu anakupatsani.chitani pangano labwino pa banja lanu komanso ndi Mulungu wanu.

Endereço

Zobue
Vila Moatize

Telefone

+258847640946

Website

Notificações

Seja o primeiro a receber as novidades e deixe-nos enviar-lhe um email quando Uthenga wa chipulumutso publica notícias e promoções. O seu endereço de email não será utilizado para qualquer outro propósito, e pode cancelar a subscrição a qualquer momento.

Entre Em Contato Com A Universidade

Envie uma mensagem para Uthenga wa chipulumutso:

Atalhos

Compartilhar

Categoria