Kulongosola yachisilamu

Kulongosola yachisilamu Ummah ujigale majiganyo gasyesyene gachisilamu

12/06/2023

{كل من عليها فان، ويبقى وجه ربك ذو الجلال والإكرام ....}

Ine ndi Inu komanso awooo tizatha koma tili nazo zija ndizakutha.

وتزودوا فإن خير الزاد التقوى

Konzekelani ndipo kukonzekera kwabwino ndiko kumuopa mulungu...

Muopeni Allah kulikonse muliko, ndipo Dziwani kuti mwacheza naye dzulo uja, utsiku wapitawu wamwalira.

Inu ndi ine tikudikila tsiku lathu lopita

Allah atipase mwayi woti tizitha kumuopa iye ndikusiya kupanga machimo mwadala.

Allahumma Ameen

اللهم أمين

08/06/2023

بسم الله الرحمن الرحيم

السلام عليكم ورحمة الله وبركاته.

Tili bwanji kulikonse tiliko??

Tikumapempha maulaliki tsiku ndi tsiku koma kokaswali osamapezekabe,

Maulaliki aja tikumatani nawo????

Funsoli aliyense ayankhe payekha payekha ndipo aliyense ayesele kuti asinthe payekha payekha.
Chifukwa mmanda muja aliyense azikayankhanso payekha payekha.

Tipemphe Allah kuti atifewetsere ndikumapanga zomutsangalatsa iye

اللهم أمين.

31/05/2023

Izi tizizikumbukila day and night.... Tizampanga mzathu komanso azatipanga amzathu

19/04/2023

بسم الله الرحمن الرحيم

السلام عليكم ورحمة الله وبركاته

Allah atilandile ibaadah yathu yomwe takhala tikupanga mmwezi ume ukutisiyawu.

Tiyeni tisayiwale kuti kuli kupeleka zakaatul fitir yomwe zolinga zake ndi:

_Kuthandiza anzathu achisilamu powapasa zakudya tsiku la Eid.

_kuyeretsa machimo ang'ono ang'ono amene takhala tikupanga mmwezi umenewu

Allah atifewetsele

09/04/2023

بسم الله الرحمن الرحيم

السلام عليكم ورحمة الله وبركاته

Muli bwanji abale ndi Alongo pamene tili mkatikati motsala kudya monga mwalamulo la Allah??

Mwezi umenewu ukhale kalasi, tikuphunzira kuchepetsa mabodza, Kuba, kukondana, kuthandizana wina ndi mzake komanso kuwerenga Quran ndikupemphela mosalekeza pomutsangalatsa Allah.

Allah atilandile kusala kwathu

آمين

21/01/2023

بسم الله الرحمن الرحيم

السلام عليكم ورحمة الله وبركاته.

Kwa amene anali ndi maganizo olakwika pakasambisidwe ka maliro, tiphunzire pamenepa

25/12/2022

بسم الله الرحمن الرحيم

السلام عليكم ورحمة الله وبركاته

الحمد لله رب العالمين والصلاة والسلام على رسول الله المبعوث رحمة للعالمين، القائل في حديثه الشريف

"من تشبه بقوم فهو منهم"

Kuyamikidwa konse ndikwa Allah, zabwino zonse za Allah zimpitile Mtumiki wathu amene kulengedwa ndikuvumbulutsidwa kwake, ndichisomo cha Allah pazolengedwa zake zonse.

Iye Mtumiki adanena kuti "amene angazifanizire ndi anthu achilunja ndiye kuti iye ali ngati omwewo"

Tiyeni tipewe komanso osatengeka ndza Christmas chifukwa sizachiphunziso chachisilamu

Allah atiteteze ndikutitalikitsa kwa Shaitwan amene ali busy pakadali pano kugwedeza mitima ya Asilamu kuti atengeke ndikupanga nawo zosalunga zomwe akupanga lero achikunjazi

Dziwaninso kuti Mtumiki Isaah (Yesu) mtendere wa Allah ukhale pa iye, sanabadwe pa 25 December ayi

Izo ndizopeka za Satana amene akukopa anthu osalungama kuti akalowe nawo limodzi kumoto

Mutalikileni, ndikutalikilanso zintchito zake

بارك الله فيكم
والسلام عليكم ورحمة الله وبركاته

17/12/2022

بسم الله الرحمن الرحيم

السلام عليكم ورحمة الله

Tiyamike Allah potisankha kukhala Asilamu amene tili ndi ndondomeko zopangila Chilichonse paumoyo wathu watsiku ndi tsiku

Timufunile zabwino zonse za Allah kuti zimpitile Mtumiki amene kubvumbulutsidwa kwake ndichisomo cha Allah pazolengedwa zonse.

Tinakamba za TWAHARA komwe ndikuziyeretsa.

Tidakambanso zamitundu yalitsilo kuti ilipo iwiri yomwenso tidayilongosola.

Mtundu woyamba ndi *LITSILO LALIKULU* limene kuziyeretsa kwake ndikusamba.

*CHISANZO CHALITSILO LALIKULU NDI JANABAH*

*KUSAMBA KWA JANABAH*

1- sambani mmanja mwanu.

2- Tsukani maliseche anu.

3-pangani udhu monga mumapangila pokaswali koma musiye *MAPAZI ANU OSACHAPA*

4- Chapani mutu wanu uku mukuwonesetsa kuti tsitsi lililonse lukhuze madzi.

5-Sambisani thupi lanulo mbali yakumanja kuyambila kumwamba mpaka pansi, *kenakonso mbali yakumanzere kuyambila kumwamba mpaka pansi*

6- kenako thilani madzi thupi lanu lonse

7- Tsukani mapazi anu munawasiya pamene mumapanga udhu aja.

*MUKATERO MWASAMBA KUSAMBA KWAJANABAH*

TITUMIZA KA VIDEO KOMWE KAKUWONESENI ZOMWE TAKAMBA APAZI WONELANI KUTI MUMVETSETSE.

13/12/2022

[12/13, 5:21 PM] Husseinchiwamuhammad@gmai: بسم الله الرحمن الرحيم

السلام عليكم ورحمة الله وبركاته

Mwaswera bwanji abale ndi Alongo kulikonse muliko?
[12/13, 5:40 PM] Husseinchiwamuhammad@gmai: Dzulo tinalongosola za *TWAHARA*

Tidanena kuti *TWAHARA* kumasulila kwake pakakhala pa chinllankhulo ndiye kuti *KUZIYERETSA*

Tsopano liwu loti *TWAHARA* tikafikano kumalamulo a chisilamu *SHARIAH* likumathanthauza kuti *KUZIYERETSA KULITSILO LILILONSE LOMWE LINGAPANGITSE KUTI SWALA ISALANDILIDWE*

Ndiye tidakamba kuti LITSILO lili mmagulu awiri makamaka LITSILO lomwe tikuliyang'ana kumbali ya TWAHARA yomwe tikuliyang'ana mbali ya Deen.

1-الحدث

2- الخبث
[12/13, 5:45 PM] Husseinchiwamuhammad@gmai: 1-الحدث

ili ndi LITSILO limene limakhala pathupi lamunthu ndipo lili mmagulunso awiri

*1...LITSILO LALIKULU*

*2......LITSILO LALING'ONO*

*🔮 LITSILO LALIKULU*

ili ndilisilo limene kuchotsa kwake ndikusamba basi
Chisanzo chake ndi JANABA(pambuyo pokumana mkazi ndimamuna wake) akuyenera onsewa kusamba kuti akhale a twahara.
[12/13, 5:49 PM] Husseinchiwamuhammad@gmai: *🔮 LITSILO LALING'ONO*

ili ndilisilo limene kuchotsa kwake ndikungopanga *UDHU* basi
Chisanzo chake ndi *kutulutsa mpweya, chimbuzi kapenanso kukoza* ukapanga chimodzi mwazimenezi kuti ukhale ndi twahara umangifunika kupanga *UDHU* basi

*NOTE*

Ngati munthu wakumana ndi mkazi wake kapena mamuna wake ndiye siudasambe kenako mkuzapanga chimbuzi kapena kukoza... Apapa ukuyenera kusamba kuti LITSILO LALIKULU lija lichoke. Ndipo siukuyenera kungopanga udhu basi ayi.
[12/13, 5:55 PM] Husseinchiwamuhammad@gmai: Izi zakambidwa apapazi KUZIYERETSA kwake timagwiritsa ntchito madzi kapena dothi ngati maziwo asowa.

*MITUNDU YA MADZI*

*MADZI ALI MMAGULU ATATU*

*1-الماء الطهور*

*2- الماء الطاهر*

*3- الماء المتنجس*

https://chat.whatsapp.com/I9kOT6M8UPwBB8gk5rTffEبسم الله الرحمن الرحيمالسلام عليكم ورحمة الله وبركاتهMALAMULO A GROUP1- ...
11/12/2022

https://chat.whatsapp.com/I9kOT6M8UPwBB8gk5rTffE

بسم الله الرحمن الرحيم

السلام عليكم ورحمة الله وبركاته

MALAMULO A GROUP

1- Akapezeka wopanga forward zilizonse azitulutsidwa kupatula ngati akufuna kufunsa Funso pazomwe wapanga forward zo.

2- Cholinga Chathu ndikuthandiza amene akufuna kuphunzira mwaulele.

3- Simalo onyozelana and tizapanga remove aliyense akubwelesa chisokonezo pakati pathu.

4- Osayankha Funso ngakhale litakuphwekelani ndicholinga choti tizipanga zinthu mwandondomeko.

5-Osafunsa mafunso amene or mutayankhidwa simungapeze phindu komanso osayankhidwa simungapeze tchimo.

6-mafunso ndiololedwa osachita MANYAZI pofunsa.

7-Tikhale ndi Niyah yofuna kupeza maphunziro.

Malamulowa azisintha pekapezeka zifukwa zoyeneretsa kuti asinthe

*من يرد الله به خيرا يفقحه في الدين*

Tikasonkhanenso KU JANNAH monga tasonkhanilana pano

اللهم أمين

WhatsApp Group Invite

https://chat.whatsapp.com/I9kOT6M8UPwBB8gk5rTffEالسلام عليكم ورحمة الله وبركاتهMwaswera bwanji abale ndi Alongo kulikons...
11/12/2022

https://chat.whatsapp.com/I9kOT6M8UPwBB8gk5rTffE

السلام عليكم ورحمة الله وبركاته

Mwaswera bwanji abale ndi Alongo kulikonse muliko

Mawa tikuyamba kukumbutsana topic ya #

Ambiri timangomva * koma sitimadziwa kuti ndichani.

Mwawa (إن شاء الله/ngati Allah angatilole) tizayendere limodzi

Koma tizangopanga ma basics kapena kuti zofunikila kuzidziwa mwapanopozo

Mugone bwino

WhatsApp Group Invite

Address

125 Pilane Street
Pretoria Central

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Kulongosola yachisilamu posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The University

Send a message to Kulongosola yachisilamu:

Share